Chidziwitso kwa ophunzira (Information for the student)

Maphunzirowa angathe kugwiritsidwa ntchito ndi ophunzira m’sukulu za pamwamba, akatswiri antchito zosiyanasiyana ndi ena onse omwe amafuna kuti azilakhula chingerezi cha bwino.

This course can be used by university students, professionals, and others who want to speak English well.

Maphunzirowa adzakuthandizani kuphunzira kulakhula chingerzi mu nthawi yochepa. Ngati mutamachita maphunzirowa mu mphindi imodzi kapena ziwiri pa tsiku pa makina ojambulira mudzatha kulakhula chingerezi chabwino m’miyezi isanu ndi umodzi okha basi. Komabe kuphunzira chingerezi kudzafunikira kudzipereka tsiku liri lonse.

These lessons will help you learn to speak English in a short period of time. If you practice one or two hours each day with the lessons on the audio recordings, you should be able to speak simple English within six months. However, learning English will require hard work each day.

Maphunzirowa akhoza kugwiritsidwa ntchito ndi ophunzira ongoyamba kumene ndi amkhala kale omwe. Maphunzirowa siwovuta kwambiri kwa ophunzira ongoyamba kumene komanso siwosavuta kwa omwe adayamba kale. Komanso akhoza kuthandiza ophunzira amene angafune kuphunzira pawokha popanda m’phunzitsi. Komabe mudzatha kuphunzira katchulidwe ka bwino ka mawu ngati mutamayesera kwa ma ola awiri pa mulungu uli wonse ndi mphunzitsi wa chingerezi.

This course can be used by both beginning and advanced English students. The lessons are neither too difficult for a beginning student nor too easy for an advanced student. They can also be used by students who want to study without an instructor. However, you will learn better pronunciation if you practice for two hours each week with an English teacher.

M’maphunzirowa muli njira zitatu zapafupi zofunika kutsatira.

There are three simple rules to follow in this English course:

  1. Muyenera kulakhula mokweza kuti muphunzire kulakhula chingerezi molondola.

    Ndi chinthu chofunika kulankhula mokweza ndi  mwachivekere mukamayesera ndi maphunziro ojambulidwa.

    1. To learn to speak English correctly, you must speak it aloud.

    It is important that you speak loudly and clearly when you are practicing with the recorded lessons.


  2. Kuphunzira kulakhula chingerezi mosadukizadukiza muyenera kumaganiza mchingerezi.

    Simukuganiza m’chingerezi ngati mukuwerenga mayankho anu. Mukangomvetsetsa ntchito iliyonse, ndi chinthu chofunika kupereka yankho mosayang’anira pena paliponse. Kukhazikika m’maganizo ndi cholinga chofuna kuganizira yankho ndi mbali yofunika pophunzira chilankhulo.

    2. To learn to speak English fluently, you must think in English.

    You are not "thinking" in English if you are reading your answers. Once you understand each exercise, it is very important that you respond without looking at the printed lesson. Making your mind work in order to think of the answer is an important part of learning a language.


  3. Mukamalankhula chingerezi chabwinomokweza nthawi ndi nthawi mudzaphunzira mofulumira kulankhula mosadukizadukiza.

    Phunziro liri lonse lidzakhala lovuta pamene wangoliyamba. Komabe mukamayesayesa mudzaphunzira kulankhula molondola. Muyenera kumayesayesa mpaka mutabwereza mosadukizadukiza popanda kuonera pa malemba. Nthawi zonse timawuza ophunzira athu, "Mudzaphunzira bwino kwambiri pamene mapirikaniro anu amva kulankhula chingerezi chabwino kuchokera pakamwa panu."

    3. The more you speak correct English aloud, the more quickly you will learn to speak fluently.

    Every lesson will be difficult when you start. However, as you practice, you will learn to speak correctly. You must practice until you can repeat the exercises fluently without looking at the printed lesson. We often tell our students, "You will learn best when your ears hear your mouth speaking correct English."


Mmene mungayambire (How to Get Started)
  1. Pochita maphunzirowa pazafunika kuti makina anu akhale ndi Acrobat Reader komanso Windows Media Player. Zonse ziwiri zikhoza kutulutsidwa mwaulere pa peji loyambirira pokhethemula pa Download PDF Reader kapena Download Media Player. Yesani kutsegula muphunziro la Download ndi kuyimba mau pa musanapite mu PDF Reader kapena Media Player. Ngati phunziro la Download silidzatseguka mudzafunikira kupeza PDF Reader. Ngati mau samveka mudzayenera kupeza Media Player.

    To use these lessons, you will need both Acrobat Reader and Windows Media Player on your computer. Both can be downloaded free from the Home page by clicking on Download PDF Reader or Download Media Player. (Try opening a "Download" lesson and playing the sound before you download either the PDF Reader or Media Player. If the "Download" lesson will not open, you need the PDF Reader. If there is no sound, you need the Media Player.)

  2. Khethemulani (kodolani) pamene pali mau oti Help kuti akufotokozereni za zizindikiro zogwiritsa ntchito mu maphunzirowa.

    2. Click on the Help link for an explanation of the icons used in the lessons.

  3. Pamene muyamba phunziro latsopano khethemulani (kodolani) chizindikiro cha Lesson Vocabulary. Sindikizani (pulintani) masamba a mau oti muwadziwe (vokabyulale). Ndipo phunzirani liwu lirilonse la chingerezi ndi kulemba tanthauzo lake mchilankhulo chanu. Lembani mau a tsopano ndimatanthauzo ake mu kabukhu kakang’ono koti mutha kuyenda nako paliponse. Unikani(bwerezani) mau anu pafupipafupi pa tsiku.

    3. When you begin a new lesson, click on the Lesson Vocabulary icon. Print the vocabulary pages. Then study each English vocabulary word and write its meaning in your language. Write new vocabulary words and expressions in a small notebook that you can carry with you. Review vocabulary frequently during the day.

  4. Khethemulani Lesson 1. Pamene Lesson 1 itseguka, khethemulani (kodolani) pa chizindikiro cha Media. Mau pa makina ojambulira adzakufunsanu kuti mumvetsera chitsanzo (“Listen to the example”). Kenako mudzamva chitsanzo cha ophunzira kuyankha mchingerezi pogwiritsa ntchito mau ojambulidwa. Zitsanzo zomwe zikupezeka m’maphunziro awiri oyambirira zikutiwonetsa momwe tingathe kamachitira pamene tikphunzira maphunzirowa. Nthawi zonse muziyesayesa maphunzirowa pakulankhula mkweza.

    4. Click on Lesson 1. When Lesson 1 opens, click on the Media icon. The voice on the audio recording will ask you to listen to the example ("Listen to the example"). Next, you will hear an example of students responding in English as they use the recording for their own English practice. The examples in the first two lessons show you how to respond as you study. Always practice the exercises by speaking out loud.

  5. Pamene muyamba phunziro latsopano mukhoza kuwerenga phunziro lolembedwa pamene mukumabwereza maphunzirowa pamakina ojambulira (otepedwa). Komabe pambuyo pakumvetsetsa phunziroli pangani maphunzirowa mosawonera pa malemba. Yeserani phunziro lirilonse mpaka mutakhoza kunena (mofanana) ndim’mene mukumvera pamakina ojambulira mopanda kuwoera pa malemba.

    5. When you begin a new lesson, you may read the written lesson as you repeat the exercises with the audio recording. However, after you understand the lesson, do the speaking exercises without looking at the written exercises. Practice each exercise until you can say it exactly as you hear it on the recording without looking at the written lesson.

  6. Ngati mukwanitsa kutero yeserani maphunzirowo pogwiritsa ntchito makina ojambulira kwa ola limodzi kapena awiri pa tsiku ndipo kwa masiku asanu pa mulungu uli wonse. (Khethemulani [Kodolani] pa See More.) Mulungu uli wonse mudzakhala ndi maola khumi ophunzira kulankhula chingerezi. Cholinga chanu mchofunikira kwambiri koposa kudziwa chabe mau ndi kuzindikira matanthauzo a mndandanda wa mau. Cholinga chanu ndi choti muthe kulankhula mndandanda wa mau mosadodomadodoma mwakuti munthu wolankhula chingerezi akhoza kuzindikira chimene mukunena mosavuta.

    6. If you are able to do so, practice the exercises using the audio recordings for one to two hours a day for five days each week. (Click on See More.) This will give you 10 hours of spoken English language study each week. Your purpose is much more than merely knowing the vocabulary words and understanding the meaning of the sentences. Your purpose is to be able speak each sentence so fluently that any English-speaking person can easily understand what you are saying.

  7. Bwerezaninso ntchito zomwe mwachita kale kumbuyo kamodzi Mulungu uli wonse.

    7. Review exercises from previous lessons once each week.

  8. Mukhoza kuyika makina ojambulira mau pafupi ndi zotulutsira mau (masipika) za kompyutala yanu kuti muthe kutepa kuti muzigwiritsa ntchito mwakufuna kwanu. Pakujambula ndi kusindikiza (kupulinta) gwiritsani ntchito mbali ya AB ya phunziro lirilonse kuchokera patsamba loyamba (homu peji) kapena gawo la Download  ya phunziro. Ngati kompyutala yanu ilibe chosungira chokwanira kutsegulira makalata onse nthawi imodzi, gwiritsani ntchito cholumikizira cha Lesson Downloads pa tsamba loyambirira ndi kujambula kapena kutulutsa kalata ili yonse padera padera. Mukhoza kujambula theka limodzi la A ku mbali imodzi ya chojambulira cha mphindi makumi asanu ndi limodzi ndinso theka lina la B ku mbali inayo. Theka loyamba la A limakhala lotalikirapo kuposa theka la mbali ya B kotero mukhoza kutembenuza nthawi yomweyo likangotha loyambalo. Mukhoza kutengera (kukopera) ma disiki a MP3 (CD) kuchokera ku Lesson Downloads pa tsamba loyamba.

    8. You can place an audio tape recorder next to your computer speakers in order to make a tape cassette copy for your personal use. For recording and printing, use the AB part of each lesson from the Home page or the "Download"   section from a lesson page. (If your computer does not have enough memory to open both documents at once, use the Lesson Downloads link on the Home page and record or print each document separately.) You can record the A half on one side of a 60-minute cassette recording tape, and the B half on the other side. The A half is always longer than the B half so that you can turn the tape over immediately after the A part is finished. You can also make MP3 compact discs (CDs) from the Lesson Downloads link on the Home page.

Cholinga cha maphunzirowa ndi kukuphunzitsani inu kulankhula chingerezi mosadodomadodoma. Maphunziro amenewa amgwiritsa ntchito mindandanda ya mau a chingerezi cha nthawi zonse. Kwa ophunzira ongoyamba kumene, njira yabwino kwambiri yophunzira kulankhula chingerezi ndi kugwiritsa ntchito ziganizo za nthawi zonse zomwe zimagwritsidwa ntchito tsiku liri lonse mu zokambirana. Kwa m,makhakale m'maphunziro, njira yabwino kwambiri yolankhulira chingerezi mosadodoma-dodoma ndikugwiritsa ntchito ziganizo zomwe zomwezo mpaka zitatchulidwa molondola. Ophunzira ongoyamba kumene pamodzi ndi oyamba kale omwe ayenera kuphunzira kulankhula ziganizo zomwe zomwezo mosadodomadodoma. Ichi ndichifukwa chake maphunziro amenewa ali ofunikira kwambiri ukamapitiriza maphuinziro. Nthawi ina ili yonse imene mukuunikiranso maphunzirowa mudzapezamo kalankhulidwe kopambana ka chingerezi chosadodomadodoma.

The purpose of this course is to teach you to speak fluent English. This course uses normal English sentences and is suitable for both beginning and advanced students. For a beginning student, the best way to learn spoken English is to use normal sentences that are used every day in conversation. For an advanced student, the best way to become fluent in English is to use these same normal sentences until they can be said correctly with good pronunciation. The difference between a beginning student and an advanced student is not in which lesson they use, but is in how much time they must spend on each lesson. This is why these lessons are so valuable for continued study. Each time you review the lessons, you will gain greater English speaking fluency.

Maphunzirowa adzakuthandizani inu kulankhula chingerezi mosadodomadodoma mu pafupipafupi theka la nthawi ya maphunziro ophunzitsa chingerezi cholankhula kuphatikiza cholemba ndi galamala. Izi nzoonadi kaya ndiwe ongoyamba kumene kapenanso ngati waphunzira chingerezi kwa zaka zambiri. Ophunzira ambiri makhala ndi vuto lalikulu kwambiri lokanika kugwiritsa ntchito verebu la chingerezi molondola. M'maphunzirowa mudzaphunzira m'mene mungagwiritsire ntchito verebu la chingerezi molondola.

These lessons will help you speak fluent English in almost half the time as courses that teach spoken English with writing and grammar. This is true whether you are just beginning or if you have studied English for many years. Most students have the greatest difficulty learning to use the English verb correctly. You will learn how to use the English verb accurately in these lessons.

Chofunika kwambiri pitirizani kubwereza maphunzirowa mpaka mutatha kunena chiganizo chilichonse mosadodomadodoma. Simunamalize maphunziro amenewa ngakhale kuti mwadziwa mau ndikuzindikira ntchito zake. Simunamalize maphunzirowa kwenikweni mpaka mutatha kugwiritsa ntchito m'ndandanda wa mauwa mu kukambirana mu chingerezi chosadodomadodoma.

Most of all, continue reviewing the lessons until you can repeat each sentence fluently. You have not yet finished the course even if you know the vocabulary and understand the exercises. You have not truly finished the course until you can use each sentence in fluent English conversation.

Tikufunirani kuphunzira chingerezi kopambana kulikonse kumene muli.

Wherever you are in the world, we wish you the best of success as you study English.

Ulendo wa munthu wanzeru: Nthano ya ophunzira chingerezi
(The Journey of a Wise Man: A Fable for English Learners)

Zofukuka za munthu wanzeru: Nthano ya ophunzira chingerezi
(A Wise Man's Discovery: A Fable for English Learners)


Lesson Text information: www.ethnicharvest.org   


www.FreeEnglishNow.com